WillowTech online mall

WillowTech online mall A Malawian online mega mall gathering Suppliers and Buyers together

Tinamva dandaulo lanu ndipo takonza
17/05/2026

Tinamva dandaulo lanu ndipo takonza

17/05/2026

To my fellow upcoming artists,

Aliyese amafuna luso lake lipite patsogolo komaso kudyerera luso lakero. Koma zindikilani k*ti for this to happen pafunika k*tsata ndondomeko zingapo k*t luso lija anthu alidziwe ndikulivomereza. Pali ma big artists muno mmalawi amene tawadziwa kumene koma adayamba zaka zingapo mbuyomo koma sankatchuka ndipo sadagwe mphwayi adapitilizabe kuyimbabe ndikunola luso lawolo. Nde ife oyamba kumene tiyeni tisathamangile k*tsogolo timange kaye maziko abwino.

Tisanayambe kugulisa nyimbo zathu kapena kukana ma show, tiyeni tichite zithu izi ndipo zizathandiza k*t athu atidziwe ndik*tilandila bwino mu music industry.

1. Tiyeni tidekhe polemba nyimbo (ngati timatha kulemba tokha nyimbo) izi zithandiza k*t information yomwe tikupeleka kugulu ikhale yachikoka, yomveka, yokhalisa komaso magulu onse a anthu akhoza kumvera nawo.

2. Kupeza beat (mental, ridim) yabwino yogwilizana ndimau kapena chamba chomwe timayimbapo bwino. Pali nyimbo zina uthenga umakhala wabwino koma poti beat sinagwilizane nyimbo yonse simabhebha.

3. Tiyeni tipange train mokwanila mawu athu komaso nyimboyo tisanapite ku studio. Osamangodalila ma sound effects chifukwa izi sizigwila mukamaimba live pa stage kapena mukamalowa freestyle.

4. Tiyeni tipeze muthu kapena athu amene angathe k*tikonza pamene talakwisa kapena kuonjezera nzeru pa nyimbo yathuyo.

5. Pezani producer wabwino ok*tha tchito amene akhoza kumakupasa direction yabwino

6. Nyimbo ikatuluka osathamagila kugulisa, inde mwaononga ndalama poimba nyimbo ija koma its an investment in your career. Komaso palibe akukudziwani nde palibe agule nyimboyo chifukwa economy yakwathukuno k*t ukagule nyimbo 5k eh pachema nde ukapezenso nyimbo inalowedwa off tune sha umakhala wazepulidwa basi. Gawani nyimboyo athu ayimvere anene zomwe akufila pa nyimboyo cholinga muphuzilepo so that your next song should be a banger

7. Mwayi wama ghetto show ukapezeka kayimbeni mukakhale akalambula bwalo kaya ndiku school, kayimbeni chifukwa that's where most of your fans are, akakufilani iwowo ndamene apangisek*ti dziko likudziweni.

8. Lowani ma group anyimbo komaso pangani upload nyimbo zanu muma website omwe safuna kuunika nyimbozo musanapange upload chifukwa amene amaunika amafuna nyimbo zokhazokhazo zoyimbidwa mwaluso nde akakupangani reject zimawawa mumafooka nde kulibwino mukamayamba kumene kumapanga upload muma website osavutawa zikayamba k*theka nde mukhoza kupanga upload kuma big website ndikuyamba kugulisa nyimbozo

Pamapeto panyimbo iliyonse yomwe mwatulusa muziphunzilapo chithu chatsopano so that your next song should be better than your previous one. Osaiwala kulimbikila (consistency) chifukwa sik*t mutchuka mawa mukayimba lelo, zitenga ndithu thawi koma osafooka.

NB: THIS MIGHT NOT WORK KWAWINA ALIYESE KOMA ZIKHOZA KUTHANDIZILA CHABE

Pali ndalama zina ku account yamuthu zimavuta k*tuluka chifukwa chakuchepa mwachitsanzo 5kwacha mungapangenayo chani cha...
03/11/2024

Pali ndalama zina ku account yamuthu zimavuta k*tuluka chifukwa chakuchepa mwachitsanzo 5kwacha mungapangenayo chani cha phindu mu 2024 ino?. Ndiye tamveselani eti what if titiyamba chipeleganyu cha dziko lamalawi muma bank mu. Tangoganizani 5kwacha pa miyezi 12 ndi 60kwacha koma ngati Bank ili ndi athu 2million ndek*t ikasungako 5kwacha mwezi umeneo muthu wamphumi mmodzi alandila 10milion. Taganizani ndichithu kapena zithu zanji zimene mukhoza kupanga zotukula moyo wanu ndi dziko lino ndi random 10million kwacha chonsecho mwangosokhako 5kwacha?

M'mawa wa Sunday lopambana.

Address

Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when WillowTech online mall posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to WillowTech online mall:

Share