08/02/2026
*KUVOMEREZANA NAYE MULUNGU*
Masalmo 133:1,3
1. Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu Kuti abale akhale pamodzi! 3. Ngati mame a ku Hermoni, Akutsikira pa mapiri a Ziyoni: Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, Ndilo moyo womka muyaya.
✅Mulungu akukondwera kuti ife okhulupilira tizikhalira pamodzi
✅Pamodzi mu pemphero,mu Uzimu,Mu chiyanjano,mu chilimbikitso,mu chikondi,mu chiphunzitso!
✅Mu umodzi timaonetsera chimene Mulungu ali....si Mulungu wa magawano/mipatiko ai.
✅Umodzi wa chikhulupiliro timalemekezana ndikukondana kweni-kweni
✅Pamene tili pamodzi mu thupi timakhalaso pamodzi mu uzimu mwathu!
✅Mulungu akaona umodzi wathu sakhala chete koma kulamulirapo dalitso ndilo moyo omka muyaya.
_MULUNGU ALI MU NTCHITO YOLIMBIKITSA UMODZI_
❌Pamene ndayamba kuganiza zoipa za munthu yemwe Mulungu wandiyanjanitsa ku uzimu ndimakhala ndasiyana naye Mulungu .
❌Zoonadi pamene NDIKUGANIZA zolimbana Ndi anthu omwe akhala akusiya zawo mkumaima nane kuti ndipambane apa ndimakhala ndikudziononga
*ZOLINGA ZA MULUNGU PA INU ZIPOSA ZOFUNA ZANU*
👌Mulungu sanagonjeko ku zofuna za anthu mkale lonse! Koma Ndi anthu omwe amagonja. Ngakhale tilimbane Ndi zomwe Mulungu akufuna pa ife zimangotitengera kuonongeka kwa zinthu zathu chifukwa zomwe Mulungu akufuna zimachitika ndithu
👌Mulungu sali monga munthu kuti akhoza kuvomera chilichonse chomwe taganiza kuti tichite....chifukwa zambiri zomwe timaziona ngati zitipatsa tsogolo Mulungu amakhala asakuonamo tsogolo,nchifukwa chake amatiletsa!
👌Maso athu nthawi zambiri amaona za apa pomwe Mulungu amaona za uko! Ndie nchifukwa chake tisanachite kalikose timayenera timufuse odziwa za uko ativomereze pa zomwe tikufuna kuchitazo.
✅"Akapanda kumanga nyumba Yehova,akuimanga aimanga chabe"(masalimo 127:1)Ngati si Mulungu akukutsogolerani pa zomwe mukufuna kuchitazo dziwani zikhala za chabe!
✅Zikufunika azikhala Mulungu pachiyambi cha ma plan athu. Ndipo zizithera Mulungu. Mamawa Wabwino