PIB Stories

PIB Stories Full of Entertainment....Just for you

Komatu Malawi uyuyu ndiye amkakoma,olo artwork yokhayo mbambande Mesaaa
21/01/2026

Komatu Malawi uyuyu ndiye amkakoma,olo artwork yokhayo mbambande Mesaaa

Panotu ndi CEO
21/01/2026

Panotu ndi CEO

20/01/2026

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Maureen Wazia Nkhoma, Ibrahim Yusuf

Atero Basitu zukhalangati mayi aja nkhonya too much!
20/01/2026

Atero Basitu zukhalangati mayi aja nkhonya too much!

Basitu akuti 2030 Chithuchi akutenga!
19/01/2026

Basitu akuti 2030 Chithuchi akutenga!

19/01/2026

Malawians forget so easily all these issues of Gettu, Feeds The World, Alice. A few days from now, it will disappear. Wait and see; the moment another story trends

15/01/2026

tamvani nkhani yanga komanso ngati mkontheka ena aziwitseniko.

Dzina langa ndiine...dzaka zanga zakubadwa 28,ndakula moyo ovutika kuti ndimalidze mamphuziro anga asekondale sizinali zomphweka,ndinadalitsika ndi lunso lamaimbidwe koma ndalama yopitira ku studio inali yondivuta kufikira pomwe mzanga wina anandiuza kuti akukajambula nyimbo ndipo ndimupelekedze.tinafika ku studio anayambapo kuimba mwina ndi mwina zimamuvuta ndipo ndinayamba kumuwunikira zomwe zinapangitsa kuti adipose mpata oimba komatu ndinaswa nyimbo ngati yanga zomwe olo ojambula zinamupasa chidwi.(fast forward)
ndinalandira unthenga kuti ndikufunika ku studio kuja nditafika ndinapedza oimba wina oziwika bwino komanso manager wake ndipo ojambula anati man takulandirani ndimakoza koza nyimbo yanu ndipo mabwanawa atamva mawu anu zawasangalatsa kotero akufuna akuloweseni mu gulu lawo,anandiuza zonse zofunika ndipo nyimbo ndinayamba kujambula ndinatchuka mukanthawi kochepa moti anthu ambiri otchuka anakhala amzanga ndalama inayamba kupedzeka moyo unasintha olo kwanthu anthu amamva kukoma,tsiku lina tinapita ku shire highlands kukaimba itantha show anati tonse tigona mkokuno kukubwera azungu amene akufuna andione mwapadera ndiomba azanga.
manager analakhula Modenkha enanu mukuziwa kale zochita,ananditengela ku room yomwe anati ndigona ndipo anati man lija ndikale munyamba kuimba nthawi yakwana kuti inunso mukhale ngati amzanuwa taonani muli gulu limodzi komano inuyo Galimoto olo nyumba mulibe,ndiye azungu omwe akubwerawa ndiwo eni Label yanthuyi ndiye ndizosavuta inuyo mungogona nawo basi mukatero ndiinu millionaire ndipo olo kunja ma show muzikaimba sinatekeseke pansi pa mtima ndinanyadira ndani safuna kugona ndi mzungu chosaziwa anali azimbambo okha okha ndipo anali owoti andigona ineyo.mmmmh ndinachita tsemwe anandiuza ngati sindilola ndisauka nyimbo zanga zilowa pansi kumbukirani kuti kangachepe komwe ndimapedza kamanthandiza azibale komanso makolo ndipo apa ndilemela kwambiri akandigona,chifukwa choopa kubwelera moyo wawumphawu ndinalolera ndipo moyo wanga unasinthiratu pano chilichose ndili nacho ndipo moyo ukufewa kunkhani yazachuma komano munthune ndatopa nalo nkhalidweli ndikufuna nditasiya chifukwa izi zimachitika kawiri kawiri maka album iliyonse isanatuluke timayenela kugonedwa ndinthu koma apa ndikufuna kusiya koma ndikuopa kuti chuma changa sichitintha?lunso langa sililowa pansi?kunena zoona ndabalalika chonde ndinthandizeni ndiyambire pati chifukwa moyo wawumphawi ndiye sindikuufunanso komanso kupembeza mafanowa sindikufuna ndikufuna moyo wa mtendere.

Pa easy tikudya uku tikumalizitsa kulemba nkhani...ikupedzani posachedwapa
15/01/2026

Pa easy tikudya uku tikumalizitsa kulemba nkhani...ikupedzani posachedwapa

14/01/2026

NOT EASY
Kodi ndinalakwanji?kodi ndichifukwa chiyani dziko limakondera achuma?monse ndinayambira muja palibe icho chisintha pamoyo wanga ndalama imangonthera chakudya changa chalero Pena kugona osadya kugona opanda chiyembekedzo kuti mwina kukamacha zisintha.Mavuto anafikapo moti tsiku ndi tsiku ndimkataya chiyembekezo kamba ka mavuto ndinasiya mamphuziro anga asekondale ndili mu form 2,ndinachoka kudzi kwanthu ku chiladzulo kulowa town ya limbe,kunena zoona ulendo olo ndinanyamuka kofikira ndinalimbe nkhumbo langa linali loti bola ndifike town.

Ndinafika chakumadzulo ndipo ndinagona pansi pa mtengo mu town yakanjeza,nthawi inanthamanga kumalo achilendo kunja kunacha poyambira panasowa olo omufunsa zakomwe ndingapedze madzi oti mkusukusula panalibe,ndinamva bwana ena akulakhula pa phone amvekele ndikubwela mpopano ndikufuna ndipedze anyamata oti atchetche kusidyaku, ndiwalakhula mwaulemu kuwauza kuti ndinganthe kuigwira tchito yonse ndenkha,anandiyang'ana mkuzati dzina lako ndani?ukusimikidzadi ungakwanise siiwe okuba iwe?ndinati ayi bwana kuba mwaine mulibe komanso dzina langa ndiine Yohane.

Tinanyamuka sanafunse zambiri mu mtima ndinasangalala kuti mulungu wandiyankha,tinafika kunyumba kwawo ndipo ganyu anayambika sinachedwe kumaliza ndalama anandipasa mosavuta chokudya ndinadya moyowu unamva kukoma pomwe anandiuza kuti ali ndizambiri zomwe zifunika waganyu kotero ngati ndingakonde ndisachoke kufikira madzulo kuti timvane zonse zoyenela popedza anali akunthamangira ku blantyre kukatenga katundu wa business yawo ndipo ndinasala pakhomo ndi mkazi wawo...

14/01/2026

Abale anga okondedwa 2026 mwamuyamba bwanji?chaka ichi tiyeni tiyendele limodzi ndipo pali zambiri zomwe ndibwele nazo

Address

Chipembere
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when PIB Stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category